Pamene mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco ndi atsogoleri a mpingo wa Orthodox akuyembekezeka kukayendera anthu othawa kwao pa chilumba la Lesbos mdziko la Greece, mkulu wa ma episkopi mdzikolo wati ali ndi mantha kamba ka kukwera kwa chiwerengero cha anthu othawa kwao omwe ali mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a Catholic Culture mkulu wa ma episkopiyu Ambuye Papamanolis wati kukwera kwa chiwerengerochi kutha kudzetsa mtopola pakati pa anthuwa.
Iwo ati kamba koti zokopa alendo ndiye njira yayikulu yopezera chuma cha dzikolo, doko lomwe anthuwa akukhala lakhala lisakulandira alendo komanso mpingo ulibe zodziyenereza zokwanira kuti upereke thandizo loyenera kwa anthuwa komabe ambuyewa anayamikira ansembe a mpingowu omwe akuyesetsa kupereka thandizo la chakudya kwa anthuwa.
Padakali pano iwo ati ali ndi mantha kuti mavutowa akakula adzetsa zamtopola pa dokopa zomwe ndi zosayenera.