Mavuto anjala ati akubwezeretsa m’mbuyo ntchito za chitukuko komanso maphunziro ku dera la kum’mwera kwa boma la Neno.
Phungu wa derali Mayi Mary Maulidi ndi omwe anena izi pomwe bungwe lina lomwe sila boma linakathandiza ena mwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala ku dera la Lisungwi kwa mfumu yayikulu Symon m’bomalo.
Mayi Maulidi ati kukula kwa vuto la njala ku dera lake kukusokoneza ntchito za chitukuko zomwe iye anakhazikitsa ku derali ponena kuti anthu akulephera kugwira ntchito chifukwa cha njala.