Mtsogoleri wa dziko laCentral African Republic, a Faustin Archangel Touadera ali ku likulu la mpingo wakatolika ku Vatican komwe akuchita zokambirana ndi mtsogoleri wa mpingo wa katolika Papa Francisko komanso akuluakulu ena ampingowu.
Malinga ndi chikalata chomwe ofesi ya zofalitsa nkhani ku Vaticanlatulutsa Presidenti-yu wakambirana za momwe chisankho chinayendera komanso momwe ntchito yokonzanso mfundo zoyendetsera dzikolo ikuyendera.
Iwo anakambirananso za kufunika koti mabungwe apitilize kuthandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi ziwawa zomwe zimachitika mdzikolo pakati pa akhristu ndi asilamu.
Presidentiyu wachitanso zokambirana ndi Mlembi wamkulu ku Vatican Cardinal Pietro Parolin komanso mlembi woona zaubale pakati pa likulu la mpingowu ndi maiko Arkiepiskopi Paul Gallagher.