Anthu othawa kwawo mazanamazana ati amira bwato lomwe anakwera litamira panyanja yaikulu ya Meditereanneanm`dziko la Egypt.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, anthu 41 ndi omwe apulumitsidwa pa ngoziyo yomwe inachitika pakati pa usiku ndipo malipoti osatsimikiza akuti anthu okwana mazana asanu ndi omwe afa koma anthu opulumutsa anzawo pangozi ati sanatsimikize za nkhaniyi.
Pakadali pano nthambi yowona za anthu othawa kwawo ku bungwe la United Nations yati chiwerengerochi ndi chachikulu kwambiri.
Chiwerengero cha anthu omwe akuthawa kwawo pogwiritsa ntchito njira za pamadzi ati chakwera chaka chino.