Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mfumu Zwelithini ya Mdziko la South Africa Ikuyembekezeka Kudzudzula Anthu Mdzikolo pa Zamtopola

$
0
0

Mfumu yachizulu Good-will Zwelithini ya mdziko la South Africa ikuyembekezeka kulankhulapo popempha mzika za dzikolo kuti zisiye kuchitira mtopola mzika za mmayiko ena zomwe zikukhala mdzikolo pa zifukwa zosiyanasiyana.

Anthu akudzudzula mfumuyo kuti ndi yomwe yayambitsa ziwembu zomwe mzika za dzikolo zikuchitira anthu a mmaiko ena, italankhula kuti anthu a mmayiko ena omwe akukhala mdzikolo abwelere mmayiko awo.

Anthu zikwizikwi akuyembekezeka kufika kubwalo la zamasewero mdera la kumvuma kwa mzinda wa Durban,komwe mfumuyo ikuyembekezeka kulankhula kwa anthu.

Iyo ikukakamira zoti anthu, anatanthauzira molakwika zomwe idalankhula.

Anthu asanu ndi awiri,ndi omwe atsimikizika kuti afa paziwembuzo.

Pakadali pano chiwerengero cha anthu omwe amangidwa pokhudzidwa ndi ziwembuzo,chafika pa mazana atatu,apolisi atamanganso anthu atatu omwe apha mzika ina ya mdziko la Mozambique mtawuni ya Alexandra posachedwapa.

Malipoti akusonyeza kuti anthu 24 mwa anthu 100 aliwonse mdzikolo, akusowa ntchito,zomwe zikuchititsa kuti adzidzudzula mzika za mmayiko ena kuti ndi zomwe zikugwira ntchito zomwe iwo akuyenera  kumagwira.

Trending Articles

Mdima unadetsa dziko

<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>