Aku likulu la chipani cha asisiteri cha Tereza Woyera mu Arkdayosizi ya Lilongwe alengeza za imfa ya Sister Fortina Saiwa.
Iwo amwalira lachiwiri ku chipatala cha Mlale m’boma la Lilongwe. Sister Saiwa anabadwa pa 10 November mchaka cha 1931 ndipo analowa m`chipanichi m`chaka cha 1953 .
Pa nthawi ya utumiki wao Sister Saiwa anakhalapo mmodzi wamkulu mwa a chipanichi kuno ku Malawi, mkulu wosula atsikana ofuna kulowa mu chipanichi komanso atumikira mmaiko a Malawi ndi Zambia.
Iwo ayikidwa m`manda pa lachinayi ku Parish ya Mlale ndipo mwambo wansembe ya Misa yotsazikana nawo udzayamba nthawi ya 10 koloko mmawa.