Mariatona ndi ndi dongosolo lapadela limene limachitika ndi cholinga chofuna kupeza ndalama, ndipo amene amakhudzidwa ndi onse woyendetsa ntchito za wailesi monga ma volunteer, abwenzi a Radio Maria komanso omvera onse, ndi cholinga chofuna kupeza ndalama zoyendetsera wailesiyi ndi ma project ena akulu akulu komanso kulipira ma bill
Liwu loti Mariatona linachokera ku Radio Maria Colombia, limene limathandauza kuyenda ndi amayi Maria ndi cholinga chofuna kupeza thandizo loyendetsera wailesi ngakhale dongosololi linayambira ku Amerika koma pano linafalikira ku maiko onse kumene kuli wayilesizi
Mariatona amatenga masiku atatu kapena kupitilira apo potengela cholinga chimene chayikidwa pa nthawiyo koma simapitilira miyezi itatu ndipo panthawiyi pamakhala maprograme apadela amene amawuulutsidwa ndi zochitika zosiyanasiyana zopezera ndalama.
Cholinga chathu Chaka Chino Ndikupedza Ndalama zosachepera 10 Million kwacha
CHOLINGA CHA RADIO MARIA NDI MARIATHON
Radio Maria sichita malonda ndipo imadalira chithandizo ndi chikondi kuchokera kwa omvera ake munjira yopeleka thandizo komanso kugwira ntchito zake . Radio Maria imadalira Chifundo cha Mulungu kudzera kwa omvera ake. Mariatona sinjira yongopezera ndalama chabe komanso ndi nthawi yodzamitsa moyo wauzimu kwa omvera ake ndi onse amathandiza Radioyi , kudzera pakutenga nawo mbali pazochitikachitika. Chachikulu ndi mapemphero.
DONGOSOLO LAKE LA MARIATONA
Dogosolo lonse la Mariatona limagawidwa munjira zitatu
a. Pre-Mariatona . iyi ndi nthawi yonkonzekera mariatona miyezi itati kapena isanu Mariatona asanachitike
b. Nthawi ya mariatona 3 days ya mariatona kapena kuposera apo
c. Nthawi imene Mariatona yatha .
UDIDO WA INU ONSE WOKONDA RADIO MARIA MALAWI
Pamene Mariatona wayamba inu omvera anthu komaso nonse wokonda Radio Maria muli ndi udindo wotenga nawo gawo pakufunafuna thandizo loyendetsera wayilesiyi
1. Pakutenga nawo gawo lofunafuna ndalama komanso malo amene tingathe kusiya ma box a Radio Maria kuti anthu aziyikamo ndalama
2. Pakutenga nawo gawo pamaprograme amene akhale akuwulutsidwa pa nyengo imeneyi ya mariatona
3. Pakuwadziwitsa anthu ena kuti nawo atenge nawo gawo pakuthandiza Radio Maria
↧