Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Unduna Upempha Anthu Asamukire Kumadera Okwera

$
0
0

Unduna woona za ulimi wa mthirira ndi chitukuko cha madzi wapempha anthu omwe akukhala m`madera otsika m`boma la Karonga kuti asamukire kumadera okwera.

 

Unduna wu wanena izi kudzera m`chikalata chomwe watulutsa  potsatira lipoti lomwe nthambi ya zanyengo  latulutsa report lomwe likuti m`bomali mugwa mvula yambiri kwa masiku asanu akudzawa yomwe ikhonza kuchitisa madzi osefukira.

 

Kudzera m`chikalatachi chomwe chasayinidwa ndi  mkulu woona za ulimi wa nthirila ndi chitukuko cha madzi, a Sandram Maweru, mvulayi ichititsa kuti mitsinje ya Songwe, North Rukuru komanso Lufilya  isefukire zomwe  ati zikhoza kuononga katundu  komanso anthu kutaya miyoyo.

M`chigawo chakumpoto mwagwa mvula yambiri yomwe yachititsa anthu ena kutaya miyoyo yawo komanso kusowa pokhala.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>