Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la Law Society ndi lokhudzidwa ndi Mavuto omwe Dziko Lino Likukumana Nawo

$
0
0

Bungwe lowona za malamulo mdziko muno la Law  Society lati ndi lokhudzidwa kwambiri ndi mavuto omwe dziko lino layamba kukumana nawo posachedwapa pankhani zosiyanasiyana.

Ena mwa mavuto omwe bungweli latchula kudzera mu lipoti lomwe latulutsa lachinai sabata ino,ndi kuchepa kwa chitetezo.

Bungweli lati ngakhale apolisi akudzipereka pantchito yosamalira miyoyo komanso katundu wa anthu, ndi zodandaulitsa powona apolisi ena akukhudzidwanso ndi milandu.

Kudzera mu lipotili bungweli ladzudzulanso mchitidwe wakupha alubino womwe wakula mdziko muno ndipo lati malamulo a dziko lino amanena momveka bwino kuti munthu aliyense ali ndi ufulu posayang’anira chilema chilichonse, ndipo lapempha boma kuti lipeze zipangizo zoyenera zomwe lingagwiritse ntchito polimbana ndi mchitidwewu.

Pamenepa bungweli lati ndilokonzeka kupereka ena mwa mamembala ake kuti athandize kuweruza milandu ya anthu oganiziridwa pa milandu yakupha ndi kuzembetsa anthuwa.

Bungweli lati ndi lokhudzidwanso kwambiri ndi zomwe zakhala zikumveka kuti mkulu wa apolisi mdziko muno adalamula apolisi kuti adziwombera ndikupheratu anthu opezeka oganiziridwa milandu yozembetsa anthu a khungu la alubino, ndipo lati likuchita chotheka kuti akuluakulu ake akumane ndi mkulu wa apolisiyu pankhaniyi.

Ilo lati langizo la mtunduwu mulibe mmalamulo adziko lino, ndipo lati malamulo adziko lino amafotokoza momveka bwino pomwe apolisi angathe kugwiritsa ntchito mfuti pantchito yawo.

Pomaliza, bungweli latinso ndi lokhudzidwa ndi ziwembu zomwe mzika za dziko la South Africa zikuchitira mzika za dziko lino ndinso maiko ena, zomwe zikukhala mdzikolo pa zifukwa zosiyanasiyana.

Lipotili lati bungweli ladzudzula kale boma la South Africa kudzera ku ofesi yake ya kazembe mdziko muno pa za ziwembuzi,ndipo lapempha dzikolo kuti lipereke chilango kwa anthu okhudzidwa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>