Msonkhano wa aphunzitsi a m’bungwe la utumiki wa ana la Tilitonse wachitika mu arkidayosizi ya mpingo wakatolika ya Lilongwe.
Ofesi yoona za ma utumiki a Papa la Pontifical Missionary Societies (PMS) mu arkidayosiziyi mogwilizana ndi ofesi yayikulu ya bungweli m’dziko muno ndi yomwe inakonza maphunzirowo.
Poyamba tawaphunzitsa kuti mabungwe a utumiki wa a Papa, PMS ndi chani ndipo kwenikweni timafuna tiwauze za limodzi mwa mabungwe a utumiki wa a Papa lomwe ndi la Holly Childhood (utumiki wa ana mu mpingo),” anatero Bambo Francis Lekaleka yemwe ndi mkulu wa ku ofesi ya bungweli mu arkidayosizi ya Lilongwe.
Bambo Lekaleka anati nthumwi zomwe zaphunzitsidwazi zikapita zikaphunzitsa ma parishi awo ma deanery ndi ma tchalitchi onse ndi cholinga choti ntchito za aphunzitsiwa zipite patsogolo.
Iwo anati cholinga chawo ndichoti anthu adziwe za bungwe la utumiki wa a Papa, ndi ntchito zake kamba koti mabungwe onse amatsamira pa bungwe limeneli kumbali yolimbitsa chikhulupiliro.
Mmodzi mwa aphunzitsi a tilitonse ku kagwa woyera parishi, Mayi Lizi Kachulu, anati msonkhanowu wawatsegula maso pa za Pontifical missionary society lomwe liri pansi pa utumiki wa a Papa.
“Lero tinazama kwambiri pa za utumiki wa ana mu mpingo. Ana adziwe chikhristu adakali aang’ono osati atakula. Izinso zatizindikiritsa kuti timakhonza pati komanso timalephera pati kuti tikakonze,”anatero Mayi Kachulu.