Ofesi ya za umoyo mu dayosizi ya mpingo wakatolika ya Zomba yalimbikitsa anthu a mdera la Chingale kuti azidzipeleka polimbana ndi mavuto a kunyentchera pakati pa ana awo.
Mlangizi wa sukulu za m’mera mpoyamba , komaso mlangizi wa ana ang’ono mu ofesiyi, Mayi Lucia Mayere Mphande, anena izi pa mwambo ophunzitsa anthu momwe angagonjetsere mavutowa kwa Chinsewu m’boma la Zomba.
Iwo anati dayosizi ya zomba mogwirizana ndi achipatala agwirana manja ndicholinga chofuna kusintha miyoyo ya ana. Zaka ziwiri zapitazi zakudya zakhala zikupezeka movutikira koma izizi zithandiza kwambiri anawa.
Patsikuli ana oposa makumi awiri (20) alandira njinga komanso mipando yomwe iwathandize kugwira ntchito zosiyana siyana.
Ndipo ofesi ya za umoyo m’boma la Zomba yayamikira dayosizi ya zomba pochepetsa ena mwa mavuto omwe anthu a mdera la Chingale ali nawo.
Mwazina patsikuli anthu anali ndi mwayi oyezetsa magazi kuti adziwe za mnthupi mwawo, kuyezetsa matenda a BP, malungo ndi shuga. Komanso amayi anali ndi mwayi oyezetsa kuti adziwe za umoyo wawo ngati ali oyembekezera.
Mwambowu unachitika pa mutu woti “Mayi wathanzi, Mwana wathanzi.”