Boma la Malawi layamikira mpingo wakatolika mdziko muno kamba kotengapo mbali pa ntchito yolimbikitsa anthu kuti azilembetsa ana awo mukaundula wa dziko lino, akabadwa.
Mkulu woyendetsa ntchito yolemba ana mu unduna wa za m’dziko a FrancisChinsinga alankhula izi pomwe bungwe la St. Egidio limatsekulira nyumba yomwe lamanga mu mzinda wa Blantyre yomwe ikhale likulu la bungweli m’dziko muno.
A Chinsinga ayamikira bungwe la St. Egidio polimbikitsa ntchito yolemba ana omwe angobadwa kumene mkaundula yomwe akuyitcha BRAVO kamba koti ntchito-yi ndi yomwe ikuthandiza kwambiri pa kaundula wa ana mdziko muno.
“Tinayamba ntchito yoti mwana aliyense akhale registered mu August 2015 mothandizidwa ndi a CDC, World Vision, UNICEF ndi mabungwe ambir, Koma dziko ndi lalikulu ana ndi ochuluka choncho kubwera kwa st Egidio kwatisangalatsa chifukwa kutithandiza kuti ntchito yolemba mkaundula ana ongobadwa kumene mpaka a zaka 16 iyende bwino komanso mwachangu,” anatero a Chinsinga.