Wolemekezeka Ambuye Julio Murat nthumwi ya a Papa m’maiko a Malawi ndi Zambia yalengeza kuti mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wasankha Reverend Fr. John Alphonsus Ryan wa chipani cha mishonale cha Patrick Woyera ngati episkopi wa dayosizi ya Mzuzu.
Nkhaniyi yalengezedwa ku likulu la mpingo ku Vatican pa 26 April, 2016 nthawi ya 12 koloko masana.
Monsinyo Micheal A. Muwowo amene amayendetsa dayosiziyi apitilirabe kugwira ntchito yawo kufikira pa nthawi imene episkopi watsopanoyu adzakhazikitsidwe.
MBIRI YA BAMBO JOHN ALPHOSUS RYAN, EPISKOPI WATSOPANO WA DAYOSIZI YA MZUZU
Bambo John Alphosus Ryan anabadwa pa 27 Febuluwale, 1952 ku Tipperary (mu Arkidayosizi ya Cashel and Emily) m’dziko la Ireland.
MAPHUNZIRO AWO
Atamaliza maphunziro awo a sekondale analowa mu chipani cha Patrick Woyera (Saint Patricks Society for Foreign Missions) imene ili ku Co Wicklow kumene anachita maphunziro a kuganiza moozama (Philosophy) komanso a zaunsembe (Theology) ku Ireland komweko. Anadzodzedwa kukhala wansembe pa 18 June, 1978.
MALO AMENE AGWIRA NTCHITO KU MALAWI KUNO
Atatumizidwa ku Malawi kuno ngati wansembe wa mishonale, Bambowo atumikira m’ma parishi osiyanasiyana mu dayosizi ya Mzuzu kuphatikizapo St. Paul ku Mzimba, St. Stephen ku Kapolo ndi St. Matias ku Misuku. Bambowa aphunzitsapo ku seminale yaing’ono ya St. Patrick’s ku Rumphi komanso ku sukulu ya sekondale yoyendera ya Misuku.
M’chaka cha 2003 anabwelera ku Ireland kukamalizitsa maphunziro awo a u Kadaulo pa Masamu mu Coding Theory.
Padakali pano Bambowa akutumikira ngati Chaplain wa sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu komwe amaphunzitsa phunziro la Masamu komanso iwowa ndi membala wa bungwe la Alangizi a bishop (Consulters) m’dayosizi ya Mzuzu.
Bambo John Alphosus Ryan amayankhula Chingerezi, Chitumbuka komanso Chindali.
Radio Maria Malawi ikufunira zabwino zonse Bambo John Alphosus Ryan omwe asankhidwa kukhala episkopi watsopano wa dayosizi ya Mzuzu.