Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PapaFrancisco wauza ansembe kuti akuyenera kutumikira anthu nthawi zonse osati kuti azikhala patsogolo kupanga mfundo zoyendetsera mpingo kaamba koti khalidwe la mtunduwu limawononga mpingo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa walankhula izi pothilirapo ndemanga pa kalata yomwe walembera ansembe a m’maiko a Latin America potsatira msonkhano omwe unachitika mmaikowa omwe unali okhudza nkhaniyi.
Mu kalatayi Papa wati akanakonda kuti zomwe mthumwi zinagwirizana ku msonkhanowu zitsatiridwe moyenera ndi cholinga choti zibereke zipatso.
Iye wapempha ansembe kuti akuyenera kuyang’anira bwino nkhosa zawo ndi kupewa kuchita zinthu zopanda tanthauzo.
Papa wauza ansembewa kuti asayiwale kuti nawonso anali anthu wamba komanso kuti mpingo sumapangidwa ndi gulu la ansembe ndi ma episkopi.