Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira asilikali omwe amagwira ntchito ya chitetezo ku likulu la mpingowu ku Vatican pa ntchito yabwino yomwe amagwira.
Papa amalankhula izi lolemba pa mwambo wolumbilitsa asilikali atsopano aku likulu la mpingowu.
Iye wati mwambowu inalinso mbali imodzi yofuna kulimbikitsa ubale wabwino potsatira mawu amene ambuye yesu analankhula akuti palibe amene ali ndi chikondi choposa ichi, popereka moyo wake kupulumutsa anzake.
Papa anapereka tanthauzo lakuti asilikaliwa ndi anthu amene amatsata mapazi a yesu khristu, amene amakonda mpingo komanso amene ali ndi chikhulupiliro cholimba.
Papa walimbikitsa asilikaliwa kuti apitilize kukhala wodzipereka pantchito yawo pokonda kulandira masacramenti, kuchita nawo misa komanso kulandira sacramenti la kulapa pafupupafupi.