Nduna ya a Papa m’mayiko a Malawi ndi Zambia , Arch-Bishop Julio Murat walimbikitsa akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno kuti atenge umwini wothandiza Radio Maria chifukwa ndi chida chodalilika mu mpingo wa katolika pofalitsa uthenga wabwino.
Ambuye Murat amalankhula izi loweruka ngati mlendo wolemekezeka pomwe Radio Maria Malawi imatsekulira Mariatona wa chaka chino ku St. Louis Montfort,Balaka Parish mu dayosizi ya Mangochi.
Ambuye Murat anati mwambowu watsegulira khomo kwa akhristu onse akufuna kwa bwino kuti athandize wailesiyi imenei kusowa chithandizo.
Mwambowu ukhala ukuchitika pa Radio Maria Malawi kuyambira pa 13 mpaka pa 15 mwezi uno ndipo udzatsekedwa pa 30 June ndi cholinga chofuna kupereka mwayi kwa onse okonda wailesi-yi kuti ayithandize.
Pa mwambowu Radio Maria Malawi ikufuna kupeza ndalama zokwana 10 million kwacha kuti ithe kukwanitsa kugwira ntchito zake bwino.