Anthu oposa 5 sauzande 800,agwidwa mu nyanja ya Mediterranean sabata yapitayi, pamene anthu ogwira ntchito yowona zachitetezo cha anthu pa nyanjayo akhwimitsa chitetezo.
Pantchitoyi achitetezowo, apeza matupi khumi a anthu omwe adafera mu nyanjayo pangozi zomwe zakhala zikuchitika masiku apitawa.
Anthuwo agwidwa mmabwato pomwe amafuna kulowa mmayiko aku Ulaya komwe amafuna kukafufuza ntchito.
Anthu oposa 1sauzande 700 afa mu nyanja ya Mediterranean chaka chino chokha pamene amafuna kulowa mmaikowa pothawa mavuto osiyanasiyana mmaiko awo.
Malipoti kusonyeza kuti anthu ena atatu,afa lamulungu lapitali bwato lomwe anakwera litamiranso munyanjayo mdziko la Egypt paulendo opita ku ulaya.