Malipoti akusonyeza kuti anthu 137 ndi omwe amwalira munyanja ya Mediterranean bwato lomwe anakwera litamira pa doko la Sicily mdziko la Italy.
Malipoti a Wailesi ya BBC ati anthu makumi ndi anayi ndi omwe apulumutsidwa pa ngoziyi lachiwiri.
Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe lowona za chisamaliro cha ana la Save the Children, wati ngoziyi inachitika la Mulungu koma chiwerengero cha anthu omwe anakhudzidwa chinali chisanadziwike.
Padakali pano anthu pafupifupi zikwi ziwiri ndi omwe amwalira podutsa nyanjayi pa ngozi zamtunduwu chaka chino chokha.