Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Fransisko Wati Mpingo Usasale Anthu Othawa Kwao

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse, Papa Fransisko, anachita zokambirana ndi atolankhani a nyuzipepala ina ya m’dziko la France komwe mwa zina wakambapo udindo wa mpingo m’maiko a ku Ulaya pa anthu othawa kwao komanso m’mene angadzetsere mgwirizano pakati pa akhristu ndi asilamu.

Papa wati mpingo m’maiko a ku Ulaya sukuyenera kusala anthu othawa kwawo a m’maiko a ku Africa  kaamba koti akukumana ndi mavuto a nkhondo, njala komanso kusowa kwa ntchito m’maiko a kwao.

Iye watinso pamene mpingo wakatolika ukuchita chaka chachifundo akhristu komanso asilamu akuyenera kuphunzira kukhalira limodzi komanso kuchitira zinthu ngati ana a banja limodzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>