Ofesi ya zamaphunziro m’boma la Balaka yati chaka chino iwonetsetsa kuti ana omwe alowe zinamwali, asakhale akadali kutsimba sukulu ikatsekulidwa mchigawo choyamba cha maphunziro a chaka chino mpaka chaka cha mawa. Mkulu owona za maphunziro m’bomalo a Paul Chiphanda ati ofesi yao, igwira ntchito limodzi ndi mafumu komanso makolo pofuna kuti m’chitidwewu uchepe chaka chino.Iye walankhula izi potsata kukula kwa chiwerengero cha ana omwe abali asanatuluke ku tsimba nthawi yotsekulira sukulu itayamba chaka chatha.
↧