Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission MEC latsimikizira anthu kuti ligwira ntchito yake mwa ukadaulo komanso mwachilungamo m’dziko muno.
Wampando wa bungweli Justice Maxson Mbendera ndi yemwe walankhula izi pa mwambo wokhazikitsa ndondomeko ya momwe bungweli ligwilire ntchito zake pokonzekera chisankho cha chaka cha mawa chomwe chidzakhale cha Aphungu, Pulezidenti komanso Makhansala. Justice Mbendera wati bungwe la MEC sililamulidwa ndi munthu aliyense kuphatikizapo boma kotero kuti ligwira ntchito yake mokomera anthu onse.