Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mabungwe A Mipingo Athandize Pa Bilu Ya Migodi

$
0
0

Bungwe la Norwegian Church Aid m’dziko muno lapempha mabungwe omwe si a boma makamaka amene ali amipingo kuti athandize boma pa ndondomeko yowunikiranso bwino bilu ya migodi.

Mkulu wa bungwe la Norwegian Church Aid, a Stain Vilumistard wanena izi pa mkumano omwe bungweli limakumana ndi mabungwe a zipembedzo zosiyanasiyana ndi cholinga chofuna kuthandiza anthu mdziko muno kumvetsa bwino udindo wawo pa nkhani za migodi.

A Villumistard ati pomwe boma likuyembekezeka kuwunikanso za biluyi, likonze mavuto omwe akuphinja eni nthaka ku madera komwe kukuchitika ntchito za migodi.

Polankhulapo, mlembi wamkulu ku  ofesi ya ku likulu la mpingo wakatolika mdziko muno  Episcopal Conference of Malawi la ECM,bambo Henry Saindi ati mkumanowu ndi wofunika kwambiri kuchitukuko cha dziko lino komanso makamaka kwa anthu omwe akukhala ku adera amene kukugwiridwa ntchito za migodi yi.

Bambo Saindi alonjeza kuti bungwe la ECM liyesetsa kuchitapo kanthu pa za biluyi ndi cholinga choti zipindulire anthu mdziko muno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>