Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Katswiri Wazisuzo ‘Izeki’ Wamwalira

$
0
0

Mmodzi mwa akatswiri azisuzo mdziko muno John Nyanga yemwe amatchuka ndi dzina loti Izeki wamwalira lamulungu masana ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth mu mzinda wa Blantyre.

Mzake yemwe amachita naye zisuzo  mu gulu la Kwathu Drama, Bon ‘Winiko’ Kalindo watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati malemuyu anagonekedwa pa chipatalachi masabata awiri apitawa.

Nyanga anatchuka kwambiri mdziko muno kudzera mu gulu la zisuzo la Kwathu pomwe amachita limodzi zisuzo ndi mzake Erick Mabedi, yemwe amatchuka ndi dzina loti Jakobo ndipo onse pamodzi amatchedwa ‘Izeki ndi Jakobo.’

Izeki wakhala akutchuka zaka zam’mbuyomu kuti wamwalira koma izi zinali nkhambakamwa chabe.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>