Parish ya mpingo wakatolika ya St. Anna ku Kapire mu dayosizi ya Mangochi yati imadziwa zakufunika kolimbikitsa moyo wauzimu pakati pa akhristu ake.
Bambo mfumu a parishi-yi bambo Danasio Malajira anena izi pakutha pa mbindikiro umene parishi-yi inakonzera akhristu ake. Mbindikirowu unayamba pa 20 May ndipo watha pa 22 May 2016.
Mbindikirowu wachitika pa mutu wakuti “Chaka Cha Chifundo, Chaka Chopempha Chifundo, Komanso Chaka Chopeleka Chifundo.” Omwe anatsogolera m’bindikirowu ndi Bambo Joseph Kimu omwenso ndi a Director a Radio Maria Malawi.
Bambo Malajira anathokoza akhristu-wa kamba ka chidwi chomwe awonetsa pofika ku mbindikiro-wu mwa unjinji wawo. Iwo ati izi zasonyeza kuti ndi akhristu olimbikira pa chikhulupiliro chawo.