Dziko la Greece layamba kusamutsa anthu ena othawa kwawo omwe amakhala pa malo ena otchedwa idomeni ndikukawaika ku malo ena kufupi ndi malire a dziko la Macedonia. Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC kusamutsa anthuwa kwachitika kaamba kofuna kuti akakhale ku malo abwino komanso otetezeka. Anthu pafupifupi 8 thousand 4 hundred omwe ambiri ndi amayi komanso ana ndiwo anali pamsasawu omwe uli kumpoto chakum`mawa kwa malire adzikolo ndi dziko la Macedonia. Anthuwa anapezeka pa malowa pamene analephera ulendo wawo opita ku maiko aku ulaya kaamba koti dziko la Macedonialinatseka chipata chomwe anthu amadutsira kupita ku maiko ena.Boma la dziko la Greece lalonjeza kuti lithandiza anthuwa powapatsa malo abwino ndi otetezeka.
↧