Anthu atatu afa kumvuma kwa dziko la Kenya potsatira ziwonetsero zosakondwa za zipani zotsutsa boma zofuna kuti bungwe loyendetsa chisankho mdzikolo lisinthe ena mwa malamulo ake.
Malipoti a wailesi ya BBC ati apolisi anawombera anthu awiri omwe amachita nawo ziwonetserozo ati pofuna kudziteteza ndipo mmodzi ati wafa kaamba koti anagwa ndi kumenyetsa mutu pomwe amathawa utsi wokhetsa misozi.
Malinga ndi malipoti sabata yatha bungwe lina lomenyera ufulu wa anthu linadzudzula apolisi mdzikolo kaamba kochita zamtopola pofuna kuthetsa ziwonetserozi.
Zipani zotsutsa bomazi ati zikufuna kuti akuluakulu oyendetsa bungwe la chisankholi atule pansi maudindo awo chisanafike chisankho cha pulezidenti chomwe chikuyembekezeka kuchitika chaka chamawa mdzikolo kaamba koti mmbuyomo akhala akukondera Pulezidenti wa dzikolo a Uhuru Kenyatta.
Ndipo polankhulapo Pulezidentiyu wati ngati zipanizi zikufuna kuti pakhale kusintha ku bungwe loyendetsa chisankho, atsatire zomwe malamulo a dzikolo amanena.