Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha akhristu kuti ngati akufuna kudzakhala oyera, sakuyenera kuchita manyazi potsatira zomwe Mulungu amafuna.
Papa amalankhula izi pa mwambo wa nsembe ya misa yomwe anachititsa ku likulu la mpingowu.
Iye wati pofuna kukwanilitsa mfundoyi akhristu akuyenera kukhala a chikhulupiliro cholimba, okonzeka kuchita zokambirana komanso azilandira chaulere chamulungu mosakakamizika.
Papa wati kuyera sikumachita kugulidwa kapena kupezedwa kaamba ka mphamvu zomwe munthu ali nazo, koma akhristu akuyenera kumalapa machimo awo, azikhala odzazidwa ndi chaulere, a chikhulupiliro komanso opanda mantha.