Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe la CFT Lakonza Ndondomeko Zokweza Malonda Mdziko Muno

$
0
0

Bungwe lowonetsetsa kuti pakukhala chilungamo pa nkhani za malonda komanso kuteteza anthu ogula m’dziko muno, la Competition and Fair Trading (CFT) lati lakonza ndondomeko za tsopano zomwe zithandize pa ntchito za malonda m’dziko muno.

M’modzi mwa akuluakulu mu bungweli m’dziko muno a Lewis Kulisewa ndi omwe  anena izi pambuyo pa mkumano wa bungweli ndi makampani omwe akuchita nawo chiwonetsero cha za malonda mu mzinda wa Blantyre.

Iwo ati bungwe lawo lakonza mfundo zatsopano zomwe zithandize pokweza ntchito za malonda m’dziko muno.

A Kulisewa adzudzulanso anthu ochita za malonda amene amakhala akunamiza anthu kuti ali ndi malonda abwino kudzera m’mauthenga omwe akumafalitsa m’ma nyuzipepala ndi njira zina zamakono.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>