M'tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PapaFrancisko wati ndi udindo wa munthu aliyense kuwonenetsetsa kuti ana akulandira chisamaliro ndi chitetezo chabwino.
Papa walankhula izi lachitatu pomwe amapeleka uthenga wake wa tsiku loganizira mtchitidwe woyipa wozembetsa ana pa dziko lonse.
Iye wati ana akuyenera kulandira chisamaliro chokwanira ndi cholinga choti asamakumane ndi mavuto osiyanasiyana okhudza moyo wawo.
Papa wapempha magulu osiyanasiyana kuti atengepo gawo popereka chitetezo pofuna kuti akhale ndi tsogolo labwino.
Tsiku loganizira mchitidwe woyipa wozembetsa ana linayamba mchaka cha 1983 potsatira kusowa kwa mwana wina wa zaka zisanu ndi chimodzi mu mzinda wa New York.