Asilikali m’dziko la Ethiopia ati akwananitsa kupulumutsa ana makumi asanu ndi atatu 53 omwe anabedwa ndi gulu lina la zigawenga m’dzikomo.
Malingana ndi malipoti a wailesi ya BBC anawa akuti anagwidwa ndi zigawengazi mwezi watha. Pomwe zigawengazi zimkachitira anawa za upanduzi akuti zinaphanso anthu ena oposera mazanaawiri (200).
M’gulu la ana omwe apulumutsidwawo akuti muli ena omwe akwanitsa miyezi itatu kuchokera tsiku lomwe anabadwa.