Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu omwe anasankha kutumikira Mulungu ngati madikoni, kuti azikhala okonzera kutumikira nthawi ina iliyonse posatengera nthawi ngakhalenso zokhumba za moyo wao.
Papa amalankhula izi lamulungu ku likulu la mpingowu ku Vatican pomwe madikoniwa amachita chaka chawo cha chifundo cha Mulungu.
Papa anawuza madikoniwa kuti sakuyenera kukhala ndi nthawi yapadera yotumikira, koma akuyenera kukhala okonzeka kutumikira nthawi ina iliyonse kamba koti nthawi ndi imodzi mwa mphatso yochokera kwa Mulungu.
Iye anati ngati akhala okonzeka kutumikira nthawi ina iliyonse, utumiki wao sukhala wodzikonda koma wofalitsa uthenga wabwino mopindula.
Mwambowu unasonkhanitsa madikoni onse omwe akutumikira mmaiko onse a pa dziko lapansi.