Dayosizi ya mpingo wakatolika ya Zomba yapempha makolo ozungulira Nyanja ya Chilwa kuti alimbikitse ana awo pa maphunziro pofuna kukonza tsogolo lawo.
Episkopi wa dayosiziyi Ambuye George Desmond Tambala alankhula izi ndi Radio Maria Malawi pomwe imafuna kudziwa zomwe dayosiziyi ikuchita polimbikitsa maphunziro a achinyamata.
“Nditapita ku chilumba cha Chisi ndinadabwa chifukwa ndinapezako anyamata ndi atsikana omwe akufunitsitsa ataphunzira sukulu ngati zathuzi koma mwayi umenewo alibe. Tiyeni tiwathandize anyamatawa aphunzire chifukwa tsogolo la dzikoli liri mmanja mwawo,” anatero Ambuye Tambala.
Ambuye Tambala anati, “Maiko ena timadabwa kuwona ana azaka 7 akuyankhula chingerezi koma kwathu kuno munthu amatha kufika fomu 4 koma kulephera kulankhula chingerezi choncho ofunika tichitepo kanthu.”
Ambuye Tambala ati mpingo ukuyesetsa kuthandiza achinyamata kuti aphunzire, koma nkofunika kuti makolo nawo akhale patsogolo pothandiza achinyamata omwe ali ndi chidwi chofuna maphunziro.