Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dziko la Kenya lati Litseka Malo Aakulu Osungirako Anthu Othawa

$
0
0

Dziko la Kenya lati litseka malo aakulu osungirako anthu othawa kwao omwe ali mdzikolo mmwezi wa November chaka chino.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC malowa omwe akusunga anthu oposera 3 hundred sauzande ambiri mwa iwo omwe ndi mzika za mdziko la Somalia, ati akuwatseka ngati mbali imodzi yofuna kupereka chitetezo kwa anthuwa ku zauchifwamba zomwe zikuchitika mdzikolo.

Boma la dzikoli lati liyesetsa kugwira ntchito limodzi ndi bungwe la mgwirizano wa maiko onse la United Nations UN komanso boma la dziko la Somalia, powapezera anthuwa malo okhala.

Malipoti ati malowa anawakhazikitsa mu chaka cha 1991 potsatira zamtopola zomwe zinkachitika mdziko la Somalia pa nthawiyo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>