Ophunzira a Form 2 msukulu za sekondale m’dziko muno ayamba lachiwiri kulemba mayeso awo a Junior Certificate of Education (JCE).
Malingana ndi ofalitsa nkhani za bungwe lowona za mayeso m’dziko muno la Malawi National Examination Board(MANEB), a Simeon Maganga, chaka chino ophunzira omwe akulemba mayeso-wa ndi oposera 143 sauzande.
Pothililapo ndemanga mulangizi wa za maphunziro mu zone ya Chitakale mayi Chimwemwe Phaiya wati mu zoniyo mayesowa ayamba bwino.
“Oyang’anira mayeso alipo okwanira komanso zipangizo zonse zogwilira ntchito ziliponso zokwanira. Pakadali pano sindinamveko kalikonse kokhuza kuti wina akufuna kubera mayeso,”anatero a Phaiya.
Iwo apemphanso ophunzirawa komanso aphunzitsi amene akuyang’anira mayesowa kuti apewe mchitidwe wobera mayeso ponena kuti adzalandira chilango chokhwima akapezeka akutero.
Chaka chino ndi chotsiriza kulemba mayesowa mdziko muno kamba koti boma lathetsa mayesowa mdziko muno tsopano.