Akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno awapempha kuti apitirize kudzipereka pa ntchito yothandiza mpingo modzidalira.
Wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Klaus Chilima ndi amene izi pa mwambo wa nsembe ya misa yotolera thandizo la ntchito pa tchalichi la Sacred Heart kuZombaCathedralmu dayosizi ya Zomba.
AChilima ati akhristu a mpingo wakatolika mdziko muno akuyenera kudziwa za udindo umene ali nawo pothandiza mpingowu ndi chuma chawo kamba koti azungu omwe anali kuthandiza mpingowu kale anabwelera kwawo.
“Mpingo uli mmanja mwa akhristu eni ake choncho aliyense mwa ife akuyenera kutengapo mbali pothandiza mmene angathere kuti mpingo wa Ambuye usagwe, usabwelere m’mbuyo koma upite patsogolo,” anatero a Chilima.
Iwo ati pamene akhristu akupereka amalandira madalitso ochuluka kamba koti chuma chimene ali nacho chimachokera kwa Mulungu.
Polankhulanso bambo mfumu a parishiyi bambo Gracious Makande anayamikira wachiwiri kwa tsogoleri wa dziko linoyu kamba kodzipereka pa ntchito zotukula mpingowu m’dziko muno ngakhale kuti nthawi zambiri amakhala otanganidwa ndi kugwira ntchito za boma.
Mwa zina wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko linoyu wapereka thandizo la zovala za ansembe pa guwa, zikho za pa misa, ndi zovala za ana othandizira misa.