Mpingo wakatolika m’dziko muno awuyamikira kamba kodzipereka pa ntchito zofalitsa uthenga wabwino.
Nduna ya zofalitsa nkhani ndi kuphunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana mayiPatricia Kaliati ndi omwe anena izi ngati mlendo wolemekezeka pa mwambo wokhazikitsa chimbale cha nyimbo zowonera cha kwayayaamayi yaSt. Symon and Jude kuChilekamumzinda waBlantyre.
Iwo ati kudzera mu zomwe amayiwa achita zasonyezelatu kuti mpingowu ukudzipeleka polimbikitsa akhristu ake pa ntchito yofalitsa uthenga wa bwino.
Polankhulanso m’modzi mwa akuluakulu omwe amayendetsa mwambowo mayiLucy Vokhiwaanati ndi okondwa kuti kwaya yawo yakwanitsa khumbo lake lotulutsa chimbalechi.
“Tikuthokoza Mulungu kamba koti zimene timafuna zachitika komanso mgwirizano womwe unalipo pakati pa amayiwa kuti zonsezi zitheke,” anatero a Vokhiwa.
Mutu wa chimbalechi ndi wakuti “Mzimu wa Ambuye Utamandike.”