M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Franciskowapempha anthu ndi akhristu a mpingowu kuti lachitatu akumbukire kupemphelera mtendere wa m’mayiko pa dziko lonse.
Malinga ndi malipoti a nyuzipepala ina ya mpingowu, Papa wati wachita izi pomwe mpingowu ukukumbukira kuti patha zaka ziwiri chikhazikitsireni m’gwilizano wa pakati pa atsogoleri a mpingowu ndi a maiko a Israel ndi Palestine opemphelera mtendere m’maiko a Aluya.
Malipoti ati mapemphero a chaka chino, anthu akuyenera kulimbikitsa mapemphero pakati pa anthu omwe akuthawa m’maiko awo kamba kosowa ntchito komanso nkhondo kuti azindikire za chikondi choposera chomwe Mulungu amakhala nacho pakati pawo.