Akhristu 49 a mpingo wakatolika akuno ku Malawi, lachitatu anakhala nawo pamwambo wamapemphero okumbukira a maritiri 22 ku Namugongo Shrine mdziko la Uganda.
Mmodzi mwa amaritiriwa Charles Lwanga Oyera adaphedwa pa 3 June 1886 pomutentha, mfumu Mwanga ya mdzikolo yomwe inkadana ndi Chikhristu italamula kuti iye ndi anzake omwe adasiya moyo wachikunja ndikulowa Chikhristu aphedwe powatentha.
Malinga ndi mbiri yampingo Charles Oyera adakanitsitsa kusiya Chikhirisitu atakakamizidwa kutero ndipo panthawi yophedwa iye adathandizira kusonkhanitsa zipangizo zomwe anthu omwe adamutentha adagwiritsa ntchito pofuna kutsimikiza chikhulupiliro chake mwa Mulungu.
Paulendo wakumalo oyerawa akhristuwa akutsogoleredwa ndi bambo Bernard Tiyesi omwe amatumikira mu Arkdayosizi ya Blantyre.