Anthu makumi atatu afa, ndipo ena 80 avulala gulu la zigawenga la Islamic State litaphulitsa mabomba awiri atinkenawo munzinda wa Baghdad m`dziko la Iraq
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC, bomba loyamba linaphulika m`dera la Shiandipo linapha anthu 19 pomwe bomba lina linaphulika pamalo ena pomwe asilikali amachitira chipikisheni a Taji kumpoto kwa mzinda wa Baghdad ndikupha anthu 11 kuphatikizapo asilikali.
Gulu la zigawengazi ati likupitiriza kuchita zamtopola munzindawu pomwe asilikali adzikoli akulimbikitsa ntchito yolanda maziko azigawengazi otchedwa Falluja omwe ali pamtunda wa makulomita 60 kumwera kwa mzinda wa Baghdad.