Bungwe la ma episkopi mdziko muno la Episcopal Conference Of Malawi [ECM] lasakha Bambo Steven Likhucha kukhala mlangizi wa apolisi mumpingowu m’dziko muno.
Bungweli lanena izi kudzera muchikalata chomwe latulutsa ndipo chasainidwa ndi mlembi wa bungweli Bambo Henry Saindi.
Bambo Likhutchaalowa m`malo mwa Bambo David Bello, omwe anapuma zaka zawo zokhalira paudindowu zitatha.
Kalatayi yatinso Bambo Likhutcha omwe ndi wamsembe otumikira ku dayosizi ya Zomba ayamba kugwira ntchito paudindowu pa 30 June chaka chino.