Ngati njira imodzi yotenga nawo gawo pa ntchito yothana ndi m`chitidwe wopha anthu a mtundu wa chi alubino, apolisi a Kanengomu m’zinda wa Lilongwe akonza ulendo wa ndawala womwe cholinga chake ndikuzindikiritsa anthu za kuipa kwa m`chitidwe wopha anthu-wa mdziko muno.
M’neneri wa apolisi pa polisi ya Kanengo, mai Salome Chibwana, wati apolisi mogwirizana ndi anthu onse ozungulira Kanengo kuphatikiza omwe ndi ma alubino, a mipingo yosiyanasiyana asing’anga komanso azipani zonse za ndale ndiwo atenge mbali pa ulendowu.
Mutu wa ndawala-yi ndi woti “Apolisi sakugwilizana ndi mchitidwe wozembetsa Komanso Kuphedwa Kwa Anthu A Chi Alubino” Ulendowu ukayambira Pa Salima Turn Off kuzungulira Area 25 ku Lilongwe ndi kukamaliza ku polisi ya Kanengo , komwe kukakhale msonkhano womaliza wozindikilitsa anthu za kuyipa kwa mchitidwe-wu m’dziko muno.