Gulu la zigawenga la Al-Shabaab lati lapha asilikali okwana makumi anayi pachiwembu chomwe linachita kumalo a asilikali a African Union m`chigawo chapakati pa dziko la Somalia.
Bungwe la AUlatsimikiza za chiwembuchi ndipo anthu omwe azungulira malowa ati anamva kulira kwa mfuti pa malowa. Asilikali abungwe la African Union akuthandiza asilikali adziko la Somalia kulimbana ndi guluri lomwe likulamulira madera osiyanasiyana m`dzikolo.
Dziko la Ethiopia ndi limodzi mwa maiko asanu omwe anatumiza asilikali ake m’dziko la Somaliakukathandiza pa ntchito yothana ndi zigawengadzi.