Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mkulu wa Bungwe la Community of Saint Egidio Mdziko Muno Wamwalira

$
0
0

Bungwe la Community of Saint Egidio lati lili mkati mokonza dongosolo la mwambo woyika m'manda yemwe anali mkulu wa bungweli m'dziko muno a Ellard Alumando.

Malemu-yi Ellard Alumando anamwalira masiku apitawa kuchipatala china m'dziko la South Africa ali mkati molandira thandizo , atakhuzidwa pa ngozi ya galimoto.

Pofotokozera Radio Maria Malawi m'modzi mwa amsembe otumikira bungweli m'dziko muno bambo Ernest Kafunsa ati pali chokonzero choti mwambo woyika m'manda thupi la malemu-yi udzachitika pa 21mwezi uno.

"Mwambo wa maliro udzachitika pa 21 June chifukwa pali alendo ochokera ku likulu lathu ku Italy omwe adzakhale nawo pa mwambowu. Amenenso adzatsogolere mwambowu ndi Bishop wa ku likulu lathu ku Vatican," anatero bambo Kafunsa.

A Kafunsa anati, "ngakhale kumudzi kwawo ndi ku Mangochi, a Allumando tiwayika ku Blantyre chifukwa ndi munthu amene wakhala akuthandiza anthu osauka ndi okalamba kwa nthawi yaitali . Iwowanso anali m'modzi mwa atsogoleri a gulu la Dream lomwe ntchito yake ndi kuthandiza anthu odwala matenda a Edzi ndi kuwapatsa mankhwala."

A Allumando anachita ngozi yagalimoto pa 28 December 2015 ndipo anapita ku chipatala china mdziko la South Africa komwe akhalako kufikira nthawi ino imene amwalira.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>