Bungwe la eni minibus m`dziko muno la Minbus Owners Association of Malawi(MOAM) lapempha boma kuti liwunikenso misonkho pofuna kuti ikhale yokomera anthu ochita malonda ang’onoang’ono omwe ambiri ndimzika za m`dziko lino. Mlembi wa mkulu wa bungweli a Coxley Kamange wanena izi poyakhula ndi Radio Maria Malawi.
Iwo ati kuwunikanso misonkhoyi kuthandiza anthu ochita malonda an`gonoan`gono kuti asamathawe misonkho.
“Mukati muwonetsetse anthu ambiri amasiya ma biziness awo kuthawa misonkho yomwe ndi yokwera kwambiri mdziko muno.. Titakumana ndi anduna tinawapempha kuti atatsitsako misonkhoyi kuti izi zisamachitike koma mpaka pano sizikusintha. Boma likanatsitsako msonkho kuti mwina ukhale pa 10% zikanachita bwino, ifeyo ndi a Malawi ndipo dzikoli ndi lathu,” anatero a Kamange.
A Kamange anadandaula kuti a Malawi omwe ndi eni dziko akuvutika kupereka misonkho yambiri zomwe zikumachititsa kuti asamapeze phindu lochuluka pa bizinezi zawo pamene anthu ena obwera monga amwenye ndi maburundi akumachita chinyengo ndikusamalipira misonkho pamapeto pake akumapeza phindu lochuluka kuposa mzika za dziko lino.