Bungwe la ma episkopi mdziko la Nigeria la Catholic Bishops’ Conference of Nigeria lapempha mzika za dzikolo kuti zipitilize kupemphelera dzikolo pofuna kuthana ndi mchitidwe wa katangale komanso ziwembu zomwe zikuchitika mdzikolo.
Bungweli lati ngakhale boma la dzikolo layesetsa kuchita chotheka kuti lithane ndi mavutowa, likuyeneranso kuti liwunikire mavuto omwe akuchitsa kuti anthu mdzikolo azikhala mwa mantha mmoyo wao wa tsiku ndi tsiku.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati bungweli lapemphanso mzika za dzikolo kuti zikhale ndi udindo polemekeza malamulo a dziko akafuna kuthetsa mavuto omwe akumana nawo.
Bungweli lati ngakhale ndi udindo wa boma wopanga malamulo, anthu akuyenera kuzindikira kuti boma silingakwanitse kuyendetsa moyo wa munthu aliyense.