Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Boma Lati Lipereka Chilango Chokhwima kwa Opezeka ndi Mlandu Wopha ma Alubino

$
0
0

M’tsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wati boma lake lionetsetsa kuti aliyense wopezeka ndi mulandu wakupha kapena kuchitira nkhanza anthu a mtundu wa chi Alubino m’dziko muno akulandira chilango chokhwima.

President Mutharika wanena izi lolemba m’boma la Kasungu pa mwambo wa tsiku loganizira anthu a chi Alubino.

Iye wati ndi wokhudzidwa kwambiri ndi kukula kwa mchitidwewu m’dziko muno.

“Ndikuthokoza nonse amene mwakhala mukutenga nawo mbali popereka malipoti a anthu oganizilidwa komanso omwe akhala akukhudzidwa ndi mchitidwe umenewu. Mupitirize kumadziwitsa apolisi koma chonde musatengere lamulo mmanja mwanu,” anatero Mutharika.

President Mutharika wapemphanso makolo omwe ali ndi ana a mtundu wa chi alubino kuti awasamalire ndi kuwateteza.

Nduna yoona kuti sipakukhala kusiyana pakati pa amuna ndi akazi pakagwilidwe ka ntchito, ana, olumala ndi chisamaliro cha wanthu, Dr. Jean Kalirani anayamikira m’tsogoleri wa dziko linoyu kamba kodzichepetsa ndi kukhala nawo pa mwambo woganizira tsikuli.

Polankhulanso pa mwambowu nthumwi ya bungwe la mgwirizano wa maiko onse la United Nations, mayi Sepa, ati dziko la Malawi likuyenera kuchita zomwe lingakwanitse pa ntchito zosamalira anthu a achi Alubino m’dziko muno, ndipo kuti thandizo la chipatala kwa anthuwa likuyenera kumapezeka mzipatala zonse maka zikuluzikulu za m’dziko muno mwa ulere.

Mwambowu patsikuli wachitika pa mutu woti “Tithetse nkhanza kwa anthu a chi alubino.”


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>