Bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace mu arkdayosizi ya LILONGWE, lati ngati dziko lino silikhala tcheru ndikulimbikitsa mchitidwe osamalira zachilengedwe, lidzakumana ndizovuta zambiri mtsogolo, maka zokhudza kusintha kwa nyengo.
Bungweli lati nchifukwa chake,layamba ntchito yophunzitsa ana msukulu zapulayimale m`boma la Salima pa momwe angasamalirire zachilengedwe ndikuonetsetsa kuti mavuto azakusintha kwa nyengo,asadzafike povuta mdziko muno.