Aphungu akunyumba yamalamulo masana ano ayamba kuvomera kupena kukana ndondomeko yazachuma yomwe nduna yazachuma idapereka kunyumbayo pa 24 mwezi watha.Pamkumanowu aphunguwa akhala akukana kapena kuvomera voti iliyonse yandondomeko yandalama zopita kumaunduna ndinso nthambi za boma.
Aphunguwa akhala akuchita izi kwa masabata awiri mpaka lachisanu sabata ya m'mawa, pomwenso nyumbayi idzakhale ikumaliza msonkhano wake.Ndalama zokwana K638.2 Billion ndi zomwe boma laika kuti zigwire ntchito chaka chino mpaka chaka cha mawa,zomwe zakwera ndi 57% kuyerekeza ndi ndondomeko ya chaka chatha yomwe inapatsidwa K406 Billion.