Bungwe la Youth Development and Productivity (YODEP)m’boma la Zomba lati ntchito yokhazikitsa ma bungwe a abambo omwe akhale akuteteza amayi ndi ana ku nkhanza zosiyanasiyana ikuyenda bwino.
Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli a Joy Mwandama ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.
Iwo ati padakali pano magulu 77 akhazikitsidwa kale kwa mfumu yaikulu Mbiza ndi Mwambo ndipo ayamba kale maphunziro.
Maphunzirowa ati athandiza abambo kuti awoneke mwatsopano pokhala patsogolo kuteteza amayi ndi ana ku nkhanza zomwe zikumakolezera matenda a Edzi.
Ntchitoyi akuyigwira ndi thandizo lochokera ku bungwe la UN-AIDS kuchokera mdziko la South Africa.