Akhristu a mpingo wakatolika mu arkidayosizi ya Blantyre awayamikira kamba kochilimika pa zampingo wodzidalira pomwe akugwira ntchito za chitukuko m`maparishi awo.
Arkiepiskopi wa dayosiziyi, Ambuye Thomas Luke Msusa, anena izi pa mwambo wansembe ya misa yodzodza adikoni awiri a mu dayosiziyi kukhala ansembe achipani cha Montfort ku parish ya Bvumbwe komanso pomwe parishiyi imakondwerela nkhoswe yake yomwe ndi Amalitiri Oyera a ku Uganda.
Ambuye Msusa ayamikira akhristu a Parishiyi omwe amanga Goloto lokongola pa iwo wokha osadalira thandizo lakunja zomwe ati zachitika kamba kakudzipereka kwawo.
“Ndikuthokoza atsogoleri a parishi ino ya Bvumbwe mogwirizana ndi atsogoleri a arkidayosizi chifukwa chotenga dzina la kudzidalira ndi kuliyika m’manja mwanu.
Iwo anayamikira anayamikira akhristuwa kamba kovomera pempho la a Papa chaka chino pamene tikukondwelera chaka cha chifundo,”anatero ambuye Msusa.
Pomaliza Ambuye Msusa alangiza akhristu kuti athandize ansembe omwe adzozedwa kumenewa powapempherera ndi kuwapatsa zosowa zawo.